Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.
Afilipi 2:4 - Buku Lopatulika munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Musamangofuna zokomera inu nokha, koma zokomeranso anzanu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Musamangofuna zokomera inu nokha koma aliyense azifuna zokomeranso ena. |
Koma chidadziwika ichi kwa Mordekai, ndiye anafotokozera Estere mkazi wamkulu; ndi Estere anamuuza mfumu, kumnenera Mordekai.
Ndipo Mose anati kwa ana a Gadi ndi ana a Rubeni, Kodi abale anu apite kunkhondo, ndi inu mukhale pansi kuno?
koma yense amene adzakhumudwitsa kamodzi ka tiana iti, takukhulupirira Ine, kumuyenera iye kuti mphero yaikulu ikolowekedwe m'khosi mwake, namizidwe poya pa nyanja.
Ndipo ife amene tili olimba tiyenera kunyamula zofooka za opanda mphamvu, ndi kusadzikondweretsa tokha.
Koma ngati muchita chikwanirire lamulolo lachifumu, monga mwa malembo, Uzikonda mnzako monga udzikonda wekha, muchita bwino: