Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Afilipi 2:27 - Buku Lopatulika

Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Pakutinso anadwaladi pafupi imfa; komatu Mulungu anamchitira chifundo; koma si iye yekha, komatu inenso, kuti ndisakhale nacho chisoni chionjezereonjezere.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Nzoonadi adaadwala zedi mpaka pafupi kufa. Mwai kuti Mulungu adamchitira chifundo. Ndipotu sadangochitira chifundo iye yekhayu, komanso ineyo, kuti chisoni changa chisakhale chosanjikizana.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zoonadi ankadwala ndipo anatsala pangʼono kumwalira. Koma Mulungu anamuchitira chifundo, ndipo sanangomuchitira chifundo iye yekhayu komanso ine, kuti chisoni changa chisachuluke.

Onani mutuwo



Afilipi 2:27
23 Mawu Ofanana  

Masiku ajawo Hezekiya anadwala, nafuna kufa. Namdzera Yesaya mneneri mwana wa Amozi, nanena naye, Atero Yehova, Siyira banja lako; pakuti udzafa, sudzakhala ndi moyo.


Adzakupulumutsa m'masautso asanu ndi limodzi; chinkana mwa asanu ndi awiri palibe choipa chidzakukhudza.


Masautso a wolungama mtima achuluka, koma Yehova amlanditsa mwa onsewa.


Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.


Taonani, ndinali ndi zowawa zazikulu, chifukwa cha mtendere wanga; Koma Inu mokonda moyo wanga, munaupulumutsa m'dzanja la chivundi, Pakuti mwaponya m'mbuyo mwanu machimo anga onse.


Pamene udulitsa pamadzi ndili pamodzi ndi iwe; ndi pooloka mitsinje sidzakukokolola; pakupyola pamoto sudzapsa; ngakhale lawi silidzakutentha.


Yehova, mundilangize, koma ndi chiweruzo; si m'mkwiyo wanu, mungandithe psiti.


Munati, Kalanga ine tsopano! Pakuti Yehova waonjezera chisoni pa zowawa zanga; ndalema ndi kubuula kwanga, sindipeza kupuma.


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Yehova, ndinamva mbiri yanu ndi mantha; Yehova, tsitsimutsani ntchito yanu pakati pa zaka, pakati pa zaka mudziwitse; pa mkwiyo mukumbukire chifundo.


Ndipo kunali m'masiku awa, kuti anadwala iye, namwalira; ndipo atamsambitsa iye anamgoneka m'chipinda chapamwamba.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


kotero kwina kuti inu mumkhululukire ndi kumtonthoza, kuti wotereyo akakamizidwe ndi chisoni chochulukacho.


popeza anali wolakalaka inu nonse, navutika mtima chifukwa mudamva kuti anadwala.


Chifukwa chake ndamtuma iye chifulumizire, kuti pakumuona mukakondwerenso, ndi inenso chindichepere chisoni.


pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine.