Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 8:18 - Buku Lopatulika

18 Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Kudandaula kwanga nkosalekeza. Mtima wanga walefukiratu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Ndadzazidwa ndi chisoni kwambiri, mtima wanga walefukiratu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 8:18
12 Mawu Ofanana  

Fulumirani ndiyankheni, Yehova; mzimu wanga ukutha. Musandibisire nkhope yanu; ndingafanane nao akutsikira kudzenje.


Chomwecho ndinati, Usandiyang'ane ine, ndilira ndi kuwawa mtima; usafulumire kunditonthoza ine, chifukwa cha kufunkhidwa kwa mwana wamkazi wa anthu anga.


Za aneneri. Mtima wanga usweka m'kati mwanga, mafupa anga onse anthunthumira; ndinga munthu woledzera, ngati munthu amene vinyo anamposa; chifukwa cha Yehova, ndi chifukwa cha mau ake opatulika.


Matumbo anga, matumbo anga! Ndipoteka pamtima panga penipeni; mtima wanga sukhala pansi m'kati mwanga; sindithai kutonthola; pakuti wamva, moyo wanga, mau a lipenga, mbiri ya nkhondo.


Tamva ife mbiri yake; manja athu alefuka, yatigwira nkhawa ndi zowawa ngati za mkazi wobala.


Ha, mutu wanga ukadakhala madzi, ndi maso anga kasupe wa misozi, kuti usana ndi usiku ndilirire ophedwa a mwana wamkazi wa anthu anga!


Chifukwa cha ichi mtima wathu ufooka, chifukwa cha izi maso athu achita chimbuuzi;


Ndinamva, ndi m'mimba mwanga munabwadamuka, milomo yanga inanthunthumira pamau, m'mafupa mwanga mudalowa chivundi, ndipo ndinanjenjemera m'malo mwanga; kuti ndipumule tsiku lamsauko, pamene akwerera anthu kuti ayambane nao ndi makamu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa