Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




Afilipi 1:16 - Buku Lopatulika

ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Otsirizaŵa amamlalika chifukwa cha chikondi, popeza kuti amadziŵa kuti Mulungu adandikhazika muno kuti ndigwire ntchito yoteteza Uthenga Wabwino.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Olalikira ndi zolinga zabwinowa amachita izi mwachikondi, podziwa kuti ine ndili muno chifukwa cha kuteteza Uthenga Wabwino.

Onani mutuwo



Afilipi 1:16
13 Mawu Ofanana  

Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga.


Iye amene akadakomoka, bwenzi lake ayenera kumchitira chifundo; angaleke kuopa Wamphamvuyonse.


Pakuti alondola amene Inu munampanda; ndipo akambirana za zowawa zao za iwo amene munawalasa.


Pakuti ngati ndichita ichi chivomerere, mphotho ndili nayo; koma ngati si chivomerere, anandikhulupirira mu udindo.


Pakuti sitikhala monga ambiriwo, akuchita malonda nao mau a Mulungu; koma monga mwa choona mtima, koma monga mwa Mulungu pamaso pa Mulungu, tilankhula mwa Khristu.


kuti mukayese inu zinthu zosiyana; kuti mukakhale a mtima woona ndi wosalakwa, kufikira tsiku la Khristu;


Koma abale, ndifuna kuti muzindikire kuti zija za kwa ine zidachita makamaka kuthandizira Uthenga Wabwino;


chifukwa cha chiyanjano chanu chakuthandizira Uthenga Wabwino, kuyambira tsiku loyambalo, kufikira tsopano lino;


monga kundiyenera ine kuyesa za inu nonse, popeza ndili nako m'mtima mwanga, kuti inu m'zomangira zanga, ndipo m'chodzikanira, ndi matsimikizidwe a Uthenga Wabwino, inu nonse muli oyanjana nane m'chisomo.


Koma muzindikira matsimikizidwe ake, kuti, monga mwana achitira atate wake, anatumikira pamodzi ndi ine Uthenga Wabwino.


Koma mudziwanso inu nokha, inu Afilipi, kuti m'chiyambi cha Uthenga Wabwino, pamene ndinachoka kutuluka mu Masedoniya, sunayanjane nane Mpingo umodzi wonse m'makhalidwe a chopereka ndi cholandira, koma inu nokha;


Inde, ndikupemphaninso, mnzanga wa m'goli woona, muthandize akazi awa amene anakangalika nane pamodzi mu Uthenga Wabwino, pamodzi ndi Klemensinso, ndi otsala aja antchito anzanga, amene maina ao ali m'buku la Moyo.