Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.
2 Samueli 9:9 - Buku Lopatulika Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pomwepo mfumu inaitana Ziba, mnyamata wa Saulo, ninena naye, Za Saulo zonse ndi za nyumba yake yonse ndampatsa mwana wa mbuye wako. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono mfumu idaitana Ziba mtumiki wa Saulo, nimuuza kuti, “Zinthu zonse zimene zidaali za Saulo ndi zonse za pa banja pake ndazipereka kwa mwana wa mbuyako Saulo. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Kenaka Davide anayitanitsa Ziba, mtumiki wa Sauli, ndipo anati, “Ine ndapereka kwa chidzukulu cha mbuye wako chilichonse chimene chinali cha Sauli ndi banja lake. |
Ndipo mfumu inati, Mwana wa mbuye wako ali kuti? Ziba nanena ndi mfumu, Onani, akhala ku Yerusalemu; pakuti anati, Lero nyumba ya Israele idzandibwezera ufumu wa atate wanga.
Pomwepo mfumu inanena ndi Ziba, Ona, za Mefiboseti zonse zili zako. Ndipo Ziba anati, Ndikulambirani, mundikomere mtima, mbuye wanga mfumu.
Ndipo mfumu inanena naye, Ulikulankhulanso bwanji za zinthu zako? Ine ndikuti, Iwe ndi Ziba mugawe dzikolo.
Ndipo Mefiboseti anati kwa mfumu, Lingakhale lonselo alitenge, popeza mbuye wanga mfumu wabwera mumtendere kunyumba yake.
Ndipo panali munthu Mbenjamini, dzina lake ndiye Kisi, mwana wa Abiyele, mwana wa Zerori, mwana wa Bekorati, mwana wa Afiya, mwana wa Mbenjamini, ndiye ngwazi.