2 Samueli 9:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Tsono iwe, ana ako ndi atumiki ako, muzidzamlimira iyeyo, ndi kumabwera ndi zinthu zokolola zakumunda, kuti banja la mbuyako likhale ndi chakudya. Koma Mefiboseti adzadya ndi ine masiku onse.” Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi atumiki 20. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri). Onani mutuwo |