Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 9:10 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Iwe ndi ana ndi antchito anu muzimulimira mʼdziko lake ndipo muzibweretsa zokololazo kuti chidzukulu cha mbuye wako chikhale ndi chakudya. Ndipo Mefiboseti, chidzukulu cha mbuye wako adzadya ndi ine nthawi zonse.” (Tsono Ziba anali ndi ana aamuna khumi ndi asanu ndi antchito makumi awiri).

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

10 Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana amuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Tsono iwe, ana ako ndi atumiki ako, muzidzamlimira iyeyo, ndi kumabwera ndi zinthu zokolola zakumunda, kuti banja la mbuyako likhale ndi chakudya. Koma Mefiboseti adzadya ndi ine masiku onse.” Ziba anali ndi ana aamuna 15 ndi atumiki 20.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 9:10
10 Mawu Ofanana  

Kenaka mfumu inafunsa kuti, “Kodi chidzukulu cha mbuye wako chili kuti?” Ziba anati kwa iye, “Watsalira ku Yerusalemu chifukwa akuganiza kuti, ‘Lero Aisraeli andibwezera ufumu wa agogo anga.’ ”


Iwo anawoloka mtsinje kukatenga banja lonse la mfumu ndi kuchita zonse zimene mfumuyo imafuna. Pamene Simei mwana wa Gera anawoloka Yorodani, anagwa pansi chafufumimba pamaso pa mfumu,


Zidzukulu zonse za agogo anga sizinayenera chilichonse koma imfa kuchokera kwa inu mbuye wanga mfumu, koma inu munapereka malo kwa mtumiki wanu pakati pa amene amadya pa tebulo lanu. Tsono ine ndili ndi chiyaninso kuti ndipitirize kudandaula kwa mfumu?”


Koma mfumu inasunga Mefiboseti mwana wa Yonatani, mwana wa Sauli, chifukwa cha kulumbira kumene mfumu Davide ndi Yonatani mwana wa Sauli anachita pamaso pa Yehova.


Davide anati kwa iye, “Usachite mantha, pakuti ndidzakuchitira ndithu chifundo chifukwa cha abambo ako Yonatani. Ine ndidzakubwezera iwe dziko lonse limene linali la agogo ako Sauli, ndipo iweyo udzadya ndi ine nthawi zonse.”


“Koma ana a Barizilai wa ku Giliyadi uwakomere mtima ndipo uwalole kuti akhale mʼgulu la anthu amene azidya pamodzi nawe. Pakuti anandisamalira pamene ndinkathawa mʼbale wako Abisalomu.


Choncho Yoyakini anavula zovala zake za ku ndende, ndipo ankadya ndi mfumu masiku onse a moyo wake.


Tsiku ndi tsiku mfumu ya ku Babuloni inkamupatsa Yehoyakini phoso lake nthawi yonse ya moyo wake, mpaka pa nthawi ya imfa yake.


Mmodzi mwa amene amadya naye atamva izi, anati kwa Yesu, “Ndi wodala munthu amene adzadye nawo mu ufumu wa Mulungu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa