Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 9:11 - Buku Lopatulika

11 Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pomwepo Ziba anati kwa mfumu, Monga mwa zonse mfumu mbuye wanga mulamulira mnyamata wanu, momwemo adzachita mnyamata wanu. Tsono Mefiboseti, anadya pa gome la Davide monga wina wa ana a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono adauza mfumu kuti, “Mtumiki wanune ndidzachita zonse potsata zimene inu mbuyanga mfumu mwalamula.” Choncho Mefiboseti ankadya ndi Davide ngati mmodzi mwa ana a mfumu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Ndipo Ziba anati kwa mfumu, “Mtumiki wanu adzachita chilichonse chimene mbuye wanga mfumu mudzalamulire wantchito wanu kuti achite.” Kotero Mefiboseti ankadya ndi Davide monga mmodzi wa ana a mfumu.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 9:11
8 Mawu Ofanana  

Ndipo anyamata a mfumu ananena kwa mfumu, Onani, monga mwa zonse mbuye wathu mfumu adzasankha, anyamata anu ndife.


Ndipo anali nao anthu chikwi chimodzi Abenjamini, ndi Ziba mnyamata wa nyumba ya Saulo; ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata ake makumi awiri pamodzi naye; iwo naoloka Yordani pamaso pa mfumu.


Ndipo Mefiboseti mwana wa Saulo anatsika kukakomana ndi mfumu; ndipo sadasambe mapazi ake, kapena kumeta ndevu zake, kapena kutsuka zovala zake kuyambira tsiku lomuka mfumu kufikira tsiku lobwera kwao mumtendere.


Ndipo anayankha, Mbuye wanga mfumu, mnyamata wanga anandinyenga; pakuti mnyamata wanu ndinati, Ndidzadzimangira bulu kuti ndiberekekepo ndi kupita ndi mfumu, pakuti mnyamata wanu ndili wopunduka.


Ndipo uzimlimira munda wake, iwe ndi ana ako ndi anyamata ako; nuzibwera nazo zipatso zake kuti mwana wa mbuye wako akhale ndi zakudya; koma Mefiboseti, mwana wa mbuye wako, adzadya pa gome langa masiku onse. Ndipo Ziba anali nao ana aamuna khumi ndi asanu, ndi anyamata makumi awiri.


Ndipo Mefiboseti anali ndi mwana wamwamuna wamng'ono, dzina lake ndiye Mika. Ndipo onse akukhala m'nyumba ya Ziba anali anyamata a Mefiboseti.


Chomwecho Mefiboseti anakhala ku Yerusalemu, pakuti anadya masiku onse ku gome la mfumu, ndipo anali wopunduka mapazi ake onse awiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa