Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 8:17 - Buku Lopatulika

ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zadoki, mwana wa Ahitubi, ndiponso Ahimeleki, mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndipo Seraya anali mlembi.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Zadoki mwana wa Ahitubi ndi Ahimeleki mwana wa Abiatara anali ansembe; Seraya anali mlembi;

Onani mutuwo



2 Samueli 8:17
21 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.


Pomwepo Husai ananena ndi Zadoki ndi Abiyatara ansembewo, Ahitofele anapangira Abisalomu ndi akulu a Israele zakutizakuti; koma ine ndinapangira zakutizakuti.


Inu ndinu abale anga, muli fupa langa ndi mnofu wanga; chifukwa ninji tsono muli am'mbuyo koposa onse kubwera nayo mfumu?


Koma ine, inde inedi mnyamata wanu, ndi Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wa Yehoyada, ndi Solomoni mnyamata wanu, sanatiitane.


Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova.


Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.


ndi Zadoki, ndiye mnyamata, ngwazi yamphamvu, ndi a nyumba ya kholo lake akulu makumi awiri mphambu awiri.


Ndi a ana a Benjamini, abale a Saulo, zikwi zitatu; pakuti mpaka pomwepo ochuluka a iwowa anaumirira nyumba ya Saulo.


Ndipo Davide anaitana Zadoki ndi Abiyatara ansembe, ndi Alevi Uriyele, Asaya, ndi Yowele, Semaya, ndi Eliyele, ndi Aminadabu, nanena nao,


ndi Zadoki wansembe, ndi abale ake ansembe, ku chihema cha Yehova, pa msanje unali ku Gibiyoni;


kupereka nsembe zopsereza kwa Yehova paguwa la nsembe zopsereza, kosalekeza, m'mawa ndi madzulo, monga mwa zonse zilembedwa m'chilamulo cha Yehova adachilamulira Israele;


Ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, anali ansembe, ndi Savisa anali mlembi,


Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,


Zadoki mwana wake, Ahimaazi mwana wake.


ndi Ahitubi anabala Zadoki, ndi Zadoki anabala Ahimaazi,


ndi Azariya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi, mtsogoleri wa m'nyumba ya Mulungu;


mwana wa Salumu, mwana wa Zadoki, mwana wa Ahitubi,


Ndipo Baruki anawerenga m'buku mau a Yeremiya m'nyumba ya Yehova, m'chipinda cha Gemariya mwana wa Safani mlembi, m'bwalo la kumtunda, pa khomo la Chipata Chatsopano cha nyumba ya Yehova, m'makutu a anthu onse.


Koma ansembe Alevi, ana a Zadoki, akusunga udikiro wa malo anga opatulika pondisokerera ana a Israele, iwowa adzandiyandikira kunditumikira Ine, nadzaima pamaso panga, kupereka mafuta ndi mwazi kwa Ine, ati Ambuye Yehova;


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?