2 Mafumu 12:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo pakuona kuti ndalama zidachuluka m'bokosimo, anakwerako mlembi wa mfumu, ndi mkulu wa ansembe, nazimanga m'matumba, naziyesa ndalama zopereka m'nyumba ya Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Nthaŵi zonse ankati akaona kuti m'bokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera kudzaŵerenga ndi kumanga m'matumba ndalama zimene zinali m'Nyumba ya Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Nthawi zonse akaona kuti mʼbokosimo muli ndalama zambiri, mlembi wa mfumu ndi mkulu wa ansembe ankabwera ndipo ankawerenga ndalama zomwe anthu ankabwera nazo ku Nyumba ya Yehova ndi kuziyika mʼmatumba. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.