Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 2:26 - Buku Lopatulika

26 Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

26 Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu masiku a Abiyatara, mkulu wa ansembe, ndipo anadya mikate yoonetsera, yosaloleka kudya ena, koma ansembe okha, ndipo anawapatsanso iwo amene anali naye?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

26 Suja adaaloŵa m'nyumba ya Mulungu, pa nthaŵi imene Abiyatara anali mkulu wa ansembe onse, nkukadya buledi woperekedwa kwa Mulungu? Chonsecho buledi ameneyo nkosaloledwa kuti wina aliyense nkumudya, kupatula ansembe okha. Komanso adaagaŵirako anzake aja amene adaali naye.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

26 Pa nthawi ya Abiatara mkulu wa ansembe, iye analowa mʼnyumba ya Mulungu ndi kudya buledi wopatulika amene amaloledwa kuti adye ndi ansembe okha. Ndipo anapereka wina kwa anzake.”

Onani mutuwo Koperani




Marko 2:26
18 Mawu Ofanana  

Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.


Chifukwa chake Zadoki ndi Abiyatara ananyamulanso likasa la Mulungu nafika nalo ku Yerusalemu. Ndipo iwo anakhala kumeneko.


Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.


ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe;


ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.


Ndipo anapangana ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi Abiyatara wansembeyo; ndipo amenewo anamtsata Adoniya namthandiza.


Ndipo mfumu Solomoni anayankha, nati kwa amai wake, Mupempheranji Abisagi wa ku Sunamu akhale wake wa Adoniya? Mumpempherenso ufumu, popeza ndiye mkulu wanga; inde ukhale wake, ndi wa Abiyatara wansembeyo, ndi wa Yowabu mwana wa Zeruya.


ndi Benaya mwana wa Yehoyada anali kazembe wa nkhondo, ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe,


Ndi Semaya mwana wa Netanele mlembi, ndiye wa Alevi, anawalembera pamaso pa mfumu; ndi akalonga, ndi Zadoki wansembe, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara, a akulu a nyumba za makolo a ansembe ndi Alevi, anatenga nyumba imodzi ya kholo lake ya Eleazara, ndi imodzi ya Itamara.


Kuti analowa m'nyumba ya Mulungu, nadya mikate yoonetsa, imene yosaloleka kudya iye kapena amene anali naye, koma ansembe okhaokha.


Ndipo ananena nao, Simunawerenge konse chimene anachichita Davide, pamene adasowa, namva njala, iye ndi iwo amene anali pamodzi naye?


Ndipo Davide anafika ku Nobu kwa Ahimeleki wansembeyo; ndipo Ahimeleki anadza kukomana ndi Davide alikunjenjemera, nanena naye, Muli nokha bwanji, palibe munthu wina nanu?


Ndipo kunali kuti Abiyatara mwana wa Ahimeleki pakuthawira kwa Davide ku Keila, anatsika ali ndi efodi m'dzanja lake.


Ndipo Davide anadziwa kuti Saulo analikulingalira zomchitira zoipa; nati kwa Abiyatara wansembe, Bwera kuno ndi efodi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa