Marko 2:27 - Buku Lopatulika27 Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201427 Ndipo ananena nao, Sabata linaikidwa chifukwa cha munthu, si munthu chifukwa cha Sabata; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa27 Tsono Yesu popitiriza mau, adauza Afarisiwo kuti, “Mulungu adaika tsiku la Sabata kuti likhale lothandiza anthu. Sadalenge anthu kuti akhale akapolo a tsiku la Sabata ai. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero27 Pamenepo anawawuza kuti, “Sabata linapangidwira munthu, osati munthu kupangidwira Sabata. Onani mutuwo |
koma tsiku lachisanu ndi chiwiri ndilo Sabata la Yehova Mulungu wako; usamagwira ntchito iliyonse, iwe, kapena mwana wako wamwamuna, kapena mwana wako wamkazi, kapena wantchito wako wamwamuna, kapena wantchito wako wamkazi, kapena ng'ombe yako, kapena bulu wako, kapena zoweta zako zilizonse, kapena mlendo wokhala m'mudzi mwako; kuti wantchito wako wamwamuna ndi wantchito wako wamkazi apumule monga iwe mwini.