Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 8:16 - Buku Lopatulika

16 Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

16 Ndipo Yowabu mwana wa Zeruya anayang'anira ankhondo, ndi Yehosafati mwana wa Ahiludi anali wolemba mbiri,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

16 Tsono Yowabu, mwana wa Zeruya, anali mtsogoleri wa ankhondo, ndipo Yehosafati, mwana wa Ahiludi, anali mlembi wolemba mbiri.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

16 Yowabu mwana wa Zeruya anali mkulu wa ankhondo; Yehosafati mwana wa Ahiludi anali mlembi wa zochitika.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 8:16
10 Mawu Ofanana  

Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.


Ndipo munene ndi Amasa, Suli fupa langa ndi mnofu wanga kodi? Mulungu andilange naonjezepo ngati sudzakhala chikhalire kazembe wa khamu la ankhondo pamaso panga, m'malo mwa Yowabu.


Ndi Yowabu mwana wa Zeruya, ndi anyamata a Davide anatuluka nakomana nao pa thamanda la Gibiyoni; nakhala pansi, ena tsidya lino, ndi ena tsidya lija la thamandalo.


Ndipo Davide anakhala mfumu ya Aisraele onse, Davide naweruza ndi chilungamo milandu ya anthu onse.


Elihorefe ndi Ahiya ana a Sisa alembi, Yehosafati mwana wa Ahiludi wolembera mbiri,


Ndipo m'mene adaitana mfumu, anawatulukira Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba ya mfumu, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolemba mbiri.


Pamenepo Eliyakimu mwana wa Hilikiya woyang'anira nyumba, ndi Sebina mlembi, ndi Yowa mwana wa Asafu wolembera mbiri, anadza kwa Hezekiya ndi zovala zao zong'ambika, namuuza mau a kazembeyo.


Nati Davide, Aliyense woyamba kukantha Ayebusi, yemweyo adzakhala mkulu ndi mtsogoleri. Nayamba kukwerako Yowabu mwana wa Zeruya, nakhala mkulu iyeyu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa