Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Mbiri 6:4 - Buku Lopatulika

4 Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Eleazara anabala Finehasi, Finehasi anabala Abisuwa,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Eleazara adabereka Finehasi, Finehasi adabereka Abisuwa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Eliezara anabereka Finehasi, Finehasi anabereka Abisuwa,

Onani mutuwo Koperani




1 Mbiri 6:4
21 Mawu Ofanana  

ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.


Ana a Merari: Mali ndi Musi. Ndi ana a Mali: Eleazara ndi Kisi.


Ana a Merari: Mali ndi Musi; mwana wa Yaziya, Beno.


Ndi ana a Amuramu: Aroni, ndi Mose, ndi Miriyamu. Ndi ana a Aroni: Nadabu, ndi Abihu, Eleazara, ndi Itamara.


Ndipo ana a Aroni ndiwo Eleazara mwana wake, Finehasi mwana wake, Abisuwa mwana wake,


ndi Finehasi mwana wa Eleazara anali mtsogoleri wao kale, ndipo Yehova anali naye.


Ndipo monga munatikhalira dzanja lokoma la Mulungu wathu, anatitengera munthu wanzeru wa ana a Mali, mwana wa Levi, mwana wa Israele; ndi Serebiya, pamodzi ndi ana ake ndi abale ake khumi mphambu asanu ndi atatu;


wa ana a Finehasi, Geresomo; wa ana a Itamara, Daniele; wa ana a Davide, Hatusi.


Ndipo Eleazara mwana wa Aroni anadzitengera mkazi wa ana aakazi a Putiyele akhale mkazi wake, ndipo anambalira Finehasi. Amenewo ndi akulu a makolo a Alevi mwa mabanja ao.


ndipo lidzakhala kwa iye, ndi kwa mbeu zake zakumtsata pangano la unsembe wosatha, popeza anachita nsanje chifukwa cha Mulungu wake, anawachitira ana a Israele chowatetezera.


Ndipo Mose anawatuma a fuko limodzi chikwi chimodzi, kunkhondo, iwowa ndi Finehasi mwana wa Eleazara wansembe, kunkhondo, ndi zipangizo zopatulika, ndi malipenga oliza m'dzanja lake.


Pamenepo Yoswa anamdalitsa, napatsa Kalebe mwana wa Yefune Hebroni likhale cholowa chake.


Koma kale dzina la Hebroni linali mzinda wa Araba, ndiye munthu wamkulu pakati pa Aanaki. Ndipo dziko linapumula nkhondo.


Ndipo ana a Israele anatumiza kwa ana a Rubeni, ndi ana a Gadi, ndi hafu la fuko la Manase, ku dziko la Giliyadi, Finehasi mwana wa Eleazara wansembe,


Eleazaranso mwana wa Aroni anafa; ndipo anamuika paphiri la Finehasi mwana wake, limene adampatsa ku mapiri a Efuremu.


namaima ku likasalo Finehasi mwana wa Eleazara mwana wa Aroni, masiku aja; nati, Kodi nditulukenso kulimbana nkhondo ndi ana a Benjamini mbale wanga, kapena ndileke? Ndipo Yehova anati, Kwerani, pakuti mawa ndidzampereka m'dzanja lako.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa