Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 15:24 - Buku Lopatulika

24 Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndipo onani, Zadoki yemwe anadza, ndi Alevi onse pamodzi naye, alikunyamula likasa la chipangano la Mulungu; natula likasa la Mulungu; ndi Abiyatara anakwera kufikira anthu onse anatha kutuluka m'mudzimo.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ansembe, Abiyatara ndi Zadoki adapita nao pamodzi ndi Alevi onse, atanyamula Bokosi lachipangano la Chauta. Adatula pansi Bokosilo, mpaka anthu onse atatuluka mumzindamo.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Zadoki anali nawonso, ndipo Alevi onse amene anali naye ananyamula Bokosi la Chipangano la Mulungu. Iwo anayika pansi Bokosi la Mulungulo ndipo Abiatara ankapereka nsembe mpaka pamene anthu onse anamaliza kutuluka mu mzinda.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 15:24
23 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu inanenanso ndi Zadoki wansembeyo, Suli mlauli kodi? Ubwere kumzinda mumtendere pamodzi ndi ana ako aamuna awiri, Ahimaazi mwana wako ndi Yonatani mwana wa Abiyatara.


Ndipo suli nao kumeneko Zadoki ndi Abiyatara ansembewo kodi? Motero chilichonse udzachimva cha m'nyumba ya mfumu uziuza Zadoki ndi Abiyatara ansembewo.


ndi Seva anali mlembi; ndi Zadoki ndi Abiyatara anali ansembe;


Ndipo kunali, pamene akunyamula likasa la Yehova atayenda mapazi asanu ndi limodzi, iye anapha nsembe ng'ombe ndi chonenepa china.


ndi Zadoki mwana wa Ahitubi, ndi Ahimeleki mwana wa Abiyatara anali ansembe, ndi Seraya anali mlembi.


Koma Zadoki wansembe, ndi Benaya mwana wake wa Yehoyada, ndi Natani mneneri, ndi Simei, ndi Rei, ndi anthu amphamvu aja adaali ndi Davide, sanali ndi Adoniya.


Ndipo mfumu inanena ndi Abiyatara wansembeyo, Pita ku Anatoti ku minda yako; pakuti wakutidwa ndi imfa; koma sindikupha iwe lero lino, chifukwa unanyamula likasa la Ambuye Yehova pamaso pa Davide atate wanga, ndi popeza unanzunzidwa monse umo atate wanga Davide anazunzidwamo.


Ndipo mfumu inaika Benaya mwana wa Yehoyada m'malo mwake kutsogolera khamu la nkhondo, ndi mfumu inaika Zadoki wansembe m'malo mwa Abiyatara.


Pamenepo Davide anati, Sayenera ena kusenza likasa la Mulungu koma Alevi ndiwo; pakuti Yehova anawasankha iwo kusenza likasa la Mulungu, ndi kumtumikira Iye kosatha.


Chidzakhala cha ansembe opatulidwa a ana a Zadoki, amene anasunga udikiro wanga osasokera, muja anasokera ana a Israele, ndi muja anasokera Alevi.


Atatha Aroni ndi ana ake aamuna kuphimba malo opatulika, ndi zipangizo zake zonse za malo opatulika, pofuna kumuka am'chigono; atatero, ana a Kohati adze kuzinyamula; koma asakhudze zopatulikazo, kuti angafe. Zinthu izi ndizo akatundu a ana a Kohati m'chihema chokomanako.


Koma sanapatse ana a Kohati kanthu; popeza ntchito yao ndiyo ya zinthu zopatulika, zimene amazisenza pa mapewa ao.


nalamulira anthu, ndi kuti, Mukadzaona likasa la chipangano la Yehova Mulungu wanu, ndi ansembe Aleviwo atalisenza, pamenepo muchoke kwanu ndi kulitsata.


Ndipo Yoswa anati kwa ansembe, Senzani likasa la chipangano, nimuoloke pamaso pa anthu. Nasenza iwo likasa la chipangano, natsogolera anthu.


Ndipo ansembe asanu ndi awiri azinyamula mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, natsogolere nazo likasa; koma tsiku lachisanu ndi chiwiri mudzizungulira mzindawo kasanu ndi kawiri, ndi ansembe aziliza mphalasazo.


Ndipo Yoswa mwana wa Nuni anaitana ansembe, nanena nao, Senzani likasa la chipangano, ndi ansembe asanu ndi awiri anyamule mphalasa zisanu ndi ziwiri zanyanga za nkhosa zamphongo, kutsogolera nazo likasa la Yehova.


Ndipo mmodzi wa ana a Ahimeleki, mwana wa Ahitubi, dzina lake ndiye Abiyatara, anapulumuka, nathawira kwa Davide.


Ndipo likasa la Mulungu linalandidwa, ndi ana awiri a Eli, Hofeni ndi Finehasi, anaphedwa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa