2 Samueli 15:23 - Buku Lopatulika23 Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201423 Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa23 Tsono anthu onse adayamba kulira mofuula pamene mfumu ndi otsatira ake ankapita. Choncho mfumuyo idaoloka mtsinjewo, ndipo anthu onse adamtsatira kupita ku chipululu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero23 Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu. Onani mutuwo |