Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
2 Samueli 6:18 - Buku Lopatulika Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamene Davide adatsiriza kupereka nsembe yopsereza ndi zoyamika, iye anawadalitsa anthuwo m'dzina la Yehova wa makamu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu m'dzina la Chauta Wamphamvuzonse. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova Wamphamvuzonse. |
Ndipo anamdalitsa iye, nati, Abramu adalitsike ndi Mulungu Wamkulukulu, mlengi wa kumwamba ndi dziko lapansi;
Ndipo anagawira anthu onse, ndiwo unyinji wonse wa Israele, amuna ndi akazi, kwa munthu yense mtanda wa mkate ndi nthuli ya nyama, ndi nchinchi ya mphesa. Ndipo anthu aja onse anabwera yense kunyumba yake.
Ndipo mfumu inapotoloka nkhope yake, nidalitsa msonkhano wonse wa Israele. Ndi msonkhano wonse wa Israele unaimirira.
Nati iye, Wolemekezeka ndi Yehova Mulungu wa Israele amene analankhula m'kamwa mwake ndi Davide atate wanga, nakwaniritsa ndi dzanja lake, nati,
Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova.
Pamenepo ansembe Alevi anauka, nadalitsa anthu; ndi mau ao anamveka, ndi pemphero lao lidakwera pokhala pake popatulika Kumwamba.
Ndipo pamene Hezekiya ndi akulu ake anadza, naona miyuluyi, analemekeza Yehova, nadalitsa anthu ake Aisraele.
Ndipo mfumu inapotolokera nkhope yake, nidalitsa khamu lonse la Israele; ndi khamu lonse la Israele linaimirira.
Angakhale opitirirapo sanena, Dalitso la Mulungu likhale pa inu; tikudalitsani m'dzina la Yehova.
Ndipo Mose anaona ntchito zonse, ndipo, taonani, adaichita monga Yehova adamuuza, momwemo adachita. Ndipo Mose anawadalitsa.
Kuyambira ndi inu, Mulungu, ataukitsa Mwana wake, anamtuma kukudalitsani inu, ndi kukubwezani yense ku zoipa zake.