1 Mbiri 16:2 - Buku Lopatulika2 Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20142 Ndipo atatha Davide kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zoyamika, anadalitsa anthu m'dzina la Yehova. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa2 Davide atamaliza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjanozo, adadalitsa anthu onse m'dzina la Chauta. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero2 Davide atatsiriza kupereka nsembe zopsereza ndi nsembe zachiyanjano, iye anadalitsa anthu mʼdzina la Yehova. Onani mutuwo |
Ndipo udindo wa kalonga ndiwo kupereka nsembe zopsereza, ndi nsembe zaufa, ndi nsembe zothira, pachikondwerero, ndi pokhala mwezi, ndi pa masabata; pa zikondwerero zonse zoikika a nyumba ya Israele; ndipo apereke nsembe yauchimo, ndi nsembe yaufa, ndi nsembe yopsereza, ndi nsembe zamtendere, kuchitira chotetezera nyumba ya Israele.