2 Samueli 23:14 - Buku Lopatulika Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali mu Betelehemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Pamenepo Davide anali m'linga, ndi boma la Afilisti linali m'Betelehemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Pamenepo nkuti Davide ali m'phanga muja, ndipo kagulu kankhondo ka Afilisti kali ku Betelehemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nthawi imeneyo Davide anali mu linga, ndipo boma la Afilisti linali ku Betelehemu. |
Koma pamene Afilisti anamva kuti adamdzoza Davide mfumu ya Israele, Afilisti onse anakwera kukafuna Davide; ndipo Davide anachimva natsikira kungaka kuja.
Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera;
Ndipo Aisraele onse anamva kunena kuti Saulo anathyola kaboma ka Afilisti, ndi kuti Afilisti anyansidwa ndi Aisraele. Ndipo anthuwo anasonkhana kwa Saulo ku Giligala.
Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka.
Motero Davide anachoka kumeneko, napulumukira ku phanga la ku Adulamu; ndipo pamene abale ake ndi banja lonse la atate wake anamva, iwo anatsikira kumeneko kwa iye.
Ndipo Davide analumbirira Saulo. Saulo namuka kwao; koma Davide ndi anthu ake anakwera kunka kungaka.