1 Samueli 14:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Yonatani ananena ndi mnyamata wonyamula zida zake, Tiye tipite ku kaboma ka osadulidwa awa; kapena Yehova adzatigwirira ntchito; pakuti palibe chomletsa Yehova kupulumutsa angakhale ndi ambiri kapena ndi owerengeka. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Yonatani adauza mnyamata wake uja kuti, “Tiye tiwolokere tipite ku kaboma kankhondo ka anthu osaumbalidwaŵa. Mwina mwake Chauta atigwirira ntchito. Pakuti palibe chomletsa Chauta kutipambanitsa ngakhale tikhale ochepa chotani.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Yonatani anawuza mnyamata wake womunyamulira zida uja kuti, “Tiye tiwoloke tipite ku kaboma ka anthu osachita mdulidwewo. Mwina Yehova adzatigwirira ntchito. Palibe chomuletsa Yehova kutipulumutsa, ngakhale tikhale ambiri kapena ochepa.” Onani mutuwo |