1 Samueli 10:5 - Buku Lopatulika5 Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumzindako mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera; Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20145 Ndipo m'tsogolo mwake mudzafika kuphiri la Mulungu, kumene kuli kaboma ka Afilisti; ndipo kudzali kuti pakufika inu kumudziko mudzakomana ndi gulu la aneneri, alikutsika kumsanje ndi chisakasa, ndi lingaka, ndi chitoliro, ndi zeze, pamaso pao; iwo adzanenera; Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa5 Pambuyo pake mufika ku phiri la Mulungu ku Gibea kumene kuli gulu lankhondo la Afilisti. Ndipo kumeneko, pamene mukuyandikira mzindawo, mukumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku kachisi ku phiri, akuimba zeze, ting'oma, chitoliro ndi pangwe, ndipo akulosa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero5 “Pambuyo pake, udzafike ku Gibeyati-Elohimu, kumene kuli gulu la ankhondo la Afilisti. Pamene ukuyandikira mzindawo, udzakumana ndi gulu la aneneri akutsika kuchokera ku phiri, akuyimba zeze, ngʼoma, zitoliro ndi pangwe, ndiponso akulosera. Onani mutuwo |