2 Samueli 22:15 - Buku Lopatulika Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza; mphezi, nawaopsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Iye anatumiza mivi, nawawaza; mphezi, nawaopsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Adaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake. Adachititsa zing'aning'ani, naŵapirikitsa. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anaponya mivi yake, nabalalitsa adani ake, ndi zingʼaningʼani zake anawagonjetsa. |
Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.
Dzuwa ndi mwezi zinaima njera mokhala mwao; pa kuunika kwa mivi yanu popita iyo. Pa kung'anipa kwa nthungo yanu yonyezimira.
Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda.
Ndipo pamene Samuele analikupereka nsembe yopserezayo, Afilisti anayandikira kuti aponyane ndi Aisraele; koma tsiku lomwe lija Yehova anagunda ndi kugunda kwakukulu pa Afilistiwo, nawapolonganitsa. Ndipo anakanthidwa pamaso pa Aisraele.