Yoswa 10:10 - Buku Lopatulika10 Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe aakulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa panjira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Ndipo Yehova anawamwaza pamaso pa Israele, ndipo anawakantha makanthidwe akulu ku Gibiyoni, nawapirikitsa pa njira yokwera pa Betehoroni, nawakantha mpaka Azeka, ndi mpaka Makeda. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Chauta adaŵachititsa mantha adaniwo pamene adangoona nkhondo ya Aisraele ija. Motero Aisraele adapambana Aamori ku Gibiyoni, naŵathamangitsa kutsika phiri la ku Betehoroni ndi kuŵakantha mpaka ku Azeka ndi ku Makeda. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Yehova anachititsa mantha adani aja atangoona gulu lankhondo la Israeli. Choncho Aisraeli anagonjetsa Aamori ku Gibiyoni ndipo anawathamangitsa mu msewu wopita ku Beti-Horoni ndi kuwapha njira yonse yopita ku Azeka ndi Makeda. Onani mutuwo |