2 Samueli 22:12 - Buku Lopatulika Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye, kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anayesa mdimawo ngati mahema omzungulira Iye, kusonkhana kwa madzi ndi mitambo yochindikira ya mlengalenga. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Mdima adausandutsa chofunda chake, mitambo yakuda yamvula adaisandutsa mwafuli wake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iye anapanga mdima kukhala chofunda chake, mitambo yakuda ya mlengalenga. |
Ndipo kunachitika, atamva Benihadadi mau awa, analikumwa nao mafumu m'misasa, ananena ndi anyamata ake, Nikani. Nandandalika pamzindapo.
Chifukwa kuti pa tsiku la tsoka Iye adzandibisa mumsasa mwake, adzandibisa mkati mwa chihema chake; pathanthwe adzandikweza.
Pomzinga pali mitambo ndi mdima; chilungamo ndi chiweruzo ndizo zolimbitsa mpando wake wachifumu.