Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 21:16 - Buku Lopatulika

Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo Isibi-Benobi, ndiye wa ana a Rafa, amene kulemera kwa mkondo wake kunali masekeli mazana atatu a mkuwa, iyeyo anavala lupanga latsopano, nati aphe Davide.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za ziphona zija zotchedwa Arefaimu, amene mkondo wake unkalemera makilogramu atatu ndi theka, ndiponso amene anali ndi lupanga latsopano m'lamba, adaganiza zoti aphe Davide.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo Isibi-Benobi, mmodzi mwa zidzukulu za Rafa, amene mkondo wake unkalemera makilogalamu atatu ndi theka ndipo analinso ndi lupanga latsopano, anati adzapha Davide.

Onani mutuwo



2 Samueli 21:16
20 Mawu Ofanana  

Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,


Padziko lapansi panali anthu akuluakulu masiku omwewo ndiponso pambuyo pake, ana aamuna a Mulungu atalowa kwa ana aakazi a anthu, ndipo anabalira iwo ana, amenewo ndiwo anthu amphamvu akalekale, anthu omveka.


Ndipo kunali chitapita ichi, kunalinso nkhondo ndi Afilisti ku Gobu; pamenepo Sibekai Muhusa anapha Safi, ndiye wa ana a Rafa.


Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa.


Awa anai anawabala ndi Rafa ku Gati; ndipo anagwa ndi dzanja la Davide ndi la anyamata ake.


Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu.


Ndipo anakwera njira ya kumwera nafika ku Hebroni; ndi apa panali Ahimani, Sesai, ndi Talimai, ana a Anaki. (Koma atamanga Hebroni zaka zisanu ndi ziwiri ndipo anamanga Zowani mu Ejipito.)


Komatu anthu okhala m'dzikomo ngamphamvu; ndi mizindayo nja malinga, yaikulu ndithu; ndipo tinaonakonso ana a Anaki.


Tikwere kuti? Abale athu atimyukitsa mitima yathu, ndi kuti, Anthuwo ndiwo aakulu ndi aatali akuposa ife; mizinda ndi yaikulu ndi ya malinga ofikira m'mwamba: tinaonakonso ana a Anaki.


(Aemimu anakhalamo kale, ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, ngati Aanaki.


Anawayesa iwonso Arefaimu, monga Aanaki; koma Amowabu awatcha Aemimu.


ndiwo anthu aakulu, ndi ambiri, ndi ataliatali, monga Aanaki; koma Yehova anawaononga pamaso pao; ndipo analanda dziko lao, nakhala m'malo mwao;


(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).


anthu aakulu ndi ataliatali, ana a Aanaki, amene muwadziwa, amene munamva mbiri yao, ndi kuti, Adzaima ndani pamaso pa ana a Anaki?


Panalibe Aanaki otsala m'dziko la ana a Israele; koma mu Gaza ndi mu Gati ndi mu Asidodi anatsalamo ena.


Ndipo Kalebe anaingitsako ana aamuna atatu a Anaki, ndiwo Sesai, ndi Ahimani, ndi Talimai, ana a Anaki.


Ndipo mtengo wa mkondo wake unali ngati mtanda woombera nsalu; ndi mutu wa mkondowo unalemera ngati masekeli mazana asanu ndi limodzi a chitsulo; ndipo womnyamulira chikopa anamtsogolera.