Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Genesis 14:5 - Buku Lopatulika

5 Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu mu Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu mu Hamu, ndi Aemimu mu Savekiriyataimu,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Chaka chakhumi ndi chinai ndipo anadza Kedorilaomere ndi mafumu amene anali naye, nawakantha Arefaimu m'Asiteroti-Karanaimu, ndi Azuzimu m'Hamu, ndi Aemimu m'Savekiriyataimu,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Pa chaka chakhumi ndi chinai Kedorilaomere pamodzi ndi anzake ogwirizana nawo, adadza ndi nkhondo nagonjetsa Arefaimu amene ankakhala ku Asiteroti-karanaimu, Azuzimu amene ankakhala ku Hamu, ndi Aemimu amene ankakhala ku chigwa cha Kiriyataimu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Mʼchaka cha khumi ndi chinayi, Kedorilaomere mogwirizana ndi mafumu ena aja anapita kukagonjetsa Arefaiwa ku Asiteroti-karanaimu, Zuzimu wa ku Hamu, Aemi wa ku Savekiriataimu

Onani mutuwo Koperani




Genesis 14:5
28 Mawu Ofanana  

Zaka khumi ndi ziwiri iwo anamtumikira Kedorilaomere, chaka chakhumi ndi chitatu anapanduka.


ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Arefaimu,


Ndipo atatu a mwa makamu atatu opambanawo, anatsika nafika kwa Davide nyengo ya kukolola m'phanga la ku Adulamu; ndi gulu la Afilisti linamanga zithando m'chigwa cha Refaimu.


Tsono Afilisti anafika natanda m'chigwa cha Refaimu.


Ndipo Afilisti anakweranso kachiwiri, natanda m'chigwa cha Refaimu.


Ndipo atatu a akulu makumi atatu anatsikira kuthanthwe kwa Davide, ku phanga la Adulamu; ndi nkhondo ya Afilisti idamanga misasa m'chigwa cha Refaimu.


Afilisti tsono anafika, nafalikira m'chigwa cha Refaimu.


Ndipo anapeza podyetsa ponenepetsa ndi pabwino, ndipo dzikoli ndi lachitando ndi lodikha ndi losungikamo, pakuti okhalako kale ndiwo a Hamu.


Pamenepo Israele analowa mu Ejipito; ndi Yakobo anakhala mlendo m'dziko la Hamu.


Anaika pakati pao zizindikiro zake, ndi zodabwitsa m'dziko la Hamu.


zodabwitsa m'dziko la Hamu, zoopsa ku Nyanja Yofiira.


Ndipo anapha ana oyamba onse a mu Ejipito, ndiwo oyamba a mphamvu yao m'mahema a Hamu.


Ndipo padzakhala ngati wamasika alikumweta tirigu wosacheka, ndi dzanja lake lilikudula ngala; inde padzakhala ngati pamene wina akunkha ngala m'chigwa cha Refaimu.


Za Mowabu. Atero Yehova wa makamu, Mulungu wa Israele: Tsoka Nebo! Pakuti wapasuka; Kiriyataimu wachitidwa manyazi, wagwidwa; linga la pamtunda lachitidwa manyazi lapasudwa.


ndi pa Kiriyataimu, ndi pa Betegamuli, ndi pa Betemeoni;


Ndipo ana a Rubeni anamanga Hesiboni, ndi Eleyale, ndi Kiriyataimu;


atakantha Sihoni mfumu ya Aamori, wakukhala mu Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya Basani, wakukhala mu Asitaroti, ku Ederei.


(Pakuti Ogi mfumu ya Basani anatsala yekha wa iwo otsalira Arefaimu; taonani, kama wake ndiye kama wachitsulo; sukhala kodi mu Raba wa ana a Amoni? Utali wake mikono isanu ndi inai, kupingasa kwake mikono inai, kuyesa mkono wa munthu).


Ndi chotsalira cha Giliyadi, ndi Basani lonse, dziko la Ogi, ndinapatsa hafu la fuko la Manase; dziko lonse la Arigobu, pamodzi ndi Basani. (Ndilo lotchedwa dziko la Arefaimu.


kufikira Yehova atapumulitsa abale anu, monga anapumulitsa inu, nalandira iwonso dziko limene Yehova Mulungu wanu awapatsa tsidya lija la Yordani; pamenepo mudzabwerera munthu yense ku cholowa chake, chimene ndinakupatsani.


Musawaopa popeza Yehova Mulungu wanu, ndiye agwirira inu nkhondo.


Nalandanso malire a Ogi mfumu ya Basani wotsala wa Arefaimu, wokhala ku Asitaroti ndi ku Ederei,


ufumu wonse wa Ogi mu Basani, wa kuchita ufumu mu Asitaroti, ndi mu Ederei (yemweyo anatsala pa otsala a Arefaimu); pakuti Mose anakantha awa, nawainga.


ndi Kiriyataimu, ndi Sibima, ndi Zeretisahara, m'phiri la kuchigwa;


ndi Giliyadi logawika pakati, ndi Asitaroti ndi Ederei, mizinda ya ufumu wa Ogi mu Basani, inali ya ana a Makiri mwana wa Manase, ndiwo ana a Makiri ogawika pakati, monga mwa mabanja ao.


ndi zonse anachitira mafumu awiri a Aamori okhala tsidya lija la Yordani, Sihoni mfumu ya ku Hesiboni, ndi Ogi mfumu ya ku Basani wokhala ku Asitaroti.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa