2 Samueli 21:20 - Buku Lopatulika20 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi padzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Ndipo panalinso nkhondo ku Gati, kumene kunali munthu wa msinkhu waukulu, amene anali nazo zala zisanu ndi chimodzi pa dzanja lonse, ndi pa phazi lonse zala zisanu ndi chimodzi, kuwerenga kwa zonse ndiko makumi awiri ndi zinai; ndipo iyenso anambala ndi Rafa. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Kudabukanso nkhondo ina ku Gati, kumene kunali munthu wina wamtali, wa zala zakumanja uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zakumwendonso uku zisanu ndi chimodzi uku zisanu ndi chimodzi, zonse pamodzi zala 24. Iyeyonso anali mmodzi mwa zidzukulu za Arefaimu. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Pa nkhondo inanso imene inachitika ku Gati panali munthu wina wamtali kwambiri wa zala zisanu ndi chimodzi mʼmanja ndi mʼmapazi ndipo zonse pamodzi zinalipo 24. Iyenso anali chidzukulu cha Rafa. Onani mutuwo |