Ndipo Davide anati, Ndidzachitira Hanuni mwana wa Nahasi zokoma, monga atate wake anandichitira ine zokoma. Chomwecho Davide anatumiza ndi dzanja la anyamata ake kuti akamsangalatse chifukwa cha atate wake. Ndipo anyamata a Davide anafika ku dziko la ana a Amoni.
Ndipo mfumu inati, Kodi atsalanso wina wa nyumba ya Saulo kuti ndimuonetsere chifundo cha Mulungu? Ziba nanena ndi mfumu, Aliponso mwana wa Yonatani wopunduka mapazi ake.