Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Rute 1:8 - Buku Lopatulika

8 Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Ndipo Naomi anati kwa apongozi ake awiri, Mukani, bwererani yense wa inu kunyumba ya amai wake; Yehova akuchitireni zokoma, monga umo munachitira akufa aja ndi ine.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Tsono Naomi adauza apongozi ake aŵiri aja kuti, “Pitani, aliyense abwerere kwa mai wake. Chauta akuchitireni zabwino, monga momwe mudachitira malemu aja ndi ine ndemwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Kenaka Naomi anati kwa apongozi ake awiri aja, “Bwererani, aliyense kwa amayi ake. Yehova akukomereni mtima, monga munachita ndi malemu aja ndi ine ndemwe.

Onani mutuwo Koperani




Rute 1:8
14 Mawu Ofanana  

Ndipo tsopano Yehova achitire inu chokoma ndi choonadi; inenso ndidzakubwezerani chokoma ichi, popeza munachita chinthuchi.


Akazi inu, mverani amuna anu a inu eni, monga kumvera Ambuye.


Akazi inu, muzimvera amuna anu, monga kuyenera mwa Ambuye.


podziwa kuti mudzalandira kwa Ambuye mphotho ya cholowa; mutumikira Ambuye Khristu mwaukapolo.


Koma Maloni ndi Kilioni anamwalira onse awiri; motero ana ake aamuna awiri ndi mwamuna wake anamsiya mkaziyo.


Natuluka iye kumene anakhalako ndi apongozi ake awiri pamodzi naye; nanka ulendo wao kubwerera ku dziko la Yuda.


Yehova akuloleni mupeze mpumulo yense m'nyumba ya mwamuna wake. Nawapsompsona, nakweza iwo mau ao nalira misozi.


Nati Naomi kwa mpongozi wake, Yehova amdalitse amene sanaleke kuwachitira zokoma amoyo ndi akufa. Ndipo Naomi ananena naye, Munthuyo ndiye mbale wathu, ndiye mmodzi wa iwo otiombolera cholowa.


Nati iye, Yehova akudalitse, mwana wanga. Chokoma chako wachichita potsiriza pano, chiposa chakuyamba chija, popeza sunatsate anyamata, angakhale osauka angakhale achuma.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa