Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
2 Samueli 19:1 - Buku Lopatulika Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anauza Yowabu, Onani mfumu ilikulira misozi, nilira Abisalomu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Anthu ena adauza Yowabu kuti, “Amfumutu akulira maliro a Abisalomu.” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Yowabu anawuzidwa kuti, “Mfumu ikulira maliro a Abisalomu.” |
Ndipo ana aamuna ake onse ndi ana aakazi onse anauka kuti amtonthoze: koma anakana kutonthozedwa; ndipo anati, Pakuti ndidzatsikira kumanda kwa mwana wanga, ndilinkulirabe. Atate wake ndipo anamlirira.
Munthuyo nanena ndi Yowabu, Ndingakhale ndikalandira ndalama chikwi m'dzanja langa, koma sindikadasamula dzanja langa pa mwana wa mfumu; pakuti m'kumva kwathu mfumu inalamulira inu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chenjerani munthu yense asakhudze mnyamatayo Abisalomu.
Pomwepo Yowabu anati, Sindiyenera kuchedwa nawe. Natenga mikondo itatu nagwaza nayo mtima wa Abisalomu alikukhala wamoyo pakati pa mtengowo.
Ndipo Yowabu ananena naye, Sudzakhala iwe wotengera mau lero, koma tsiku lina udzatengera mau; koma lero sudzatengera mau, chifukwa mwana wa mfumu wafa.
Ndipo mfumuyo inagwidwa chisoni, nikwera ku chipinda chosanja pa chipatacho, nilira misozi; niyenda, nitero, Mwana wanga Abisalomu, mwana wanga Abisalomu; mwana wanga! Mwenzi nditakufera ine, Abisalomu, mwana wanga, mwana wanga!
Ndipo mfumu inalamulira Yowabu ndi Abisai ndi Itai, kuti, Chifukwa cha ine muchite mofatsa ndi mnyamatayo, Abisalomu. Ndipo anthu onse anamva pamene mfumu inalamulira atsogoleriwo za Abisalomu.
Ndipo chipulumutso cha tsiku lija chinasandulika maliro kwa anthu onse; pakuti anthu anamva kuti, Mfumu ili ndi chisoni chifukwa cha mwana wake.
Ndipo ndidzatsanulira pa nyumba ya Davide, ndi pa okhala mu Yerusalemu, mzimu wa chisomo ndi wakupembedza; ndipo adzandipenyera Ine amene anandipyoza; nadzamlira ngati munthu alira mwana wake mmodzi yekha, nadzammvera zowawa mtima, monga munthu amvera zowawa mtima mwana wake woyamba.