Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;
2 Samueli 18:17 - Buku Lopatulika Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo anatenga Abisalomu namponya m'chidzenje chachikulu kunkhalangoko; naunjika pamwamba pake mulu waukulu ndithu wamiyala; ndipo Aisraele onse anathawa yense ku hema wake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndipo ankhondowo adatenga mtembo wa Abisalomu, nakautaya m'chidzenje chachikulu m'nkhalango, naunjika mulu wa miyala padzenjepo. Aisraele onse adathaŵa, aliyense kuthaŵira kwao. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Iwo anatenga Abisalomu ndi kumuponya mʼdzenje lalikulu mʼchipululumo ndipo anawunjikapo miyala ikuluikulu. Nthawiyi Aisraeli onse anathawa kupita ku nyumba zawo. |
Ndipo Yowabu anafika kunyumba ya mfumu, nati, Lero mwachititsa manyazi nkhope zao za anyamata anu onse, amene anapulumutsa moyo wanu lero, ndi miyoyo ya ana anu aamuna ndi aakazi, ndi miyoyo ya akazi anu, ndi miyoyo ya akazi anu aang'ono;
Pamenepo mfumu inanyamuka, nikakhala pachipata. Ndipo anauza anthu kuti, Onani mfumu ilikukhala pachipata; anthu onse nadza pamaso pa mfumu. Koma Aisraele adathawa, munthu yense ku hema wake.
Ndipo anthu onse a m'mafuko onse a Israele analikutsutsana, ndi kuti, Mfumuyo inatilanditsa ife m'dzanja la adani athu, natipulumutsa m'dzanja la Afilisti; ndipo tsopano inathawa m'dziko kuthawa Abisalomu.
Ndipo kudangotero kuti pamenepo panali munthu woipa, dzina lake ndiye Sheba mwana wa Bikiri Mbenjamini; naliza iye lipenga, nati, Ife tilibe gawo mwa Davide, tilibenso cholowa mwa mwana wa Yese; munthu yense apite ku mahema ake, Israele inu.
Pomwepo mkaziyo anapita kwa anthu onse mwa nzeru yake. Ndipo iwo anadula mutu wa Sheba mwana wa Bikiri, nauponya kunja kwa Yowabu. Ndipo analiza lipenga, nabalalika kuchoka mumzindamo, munthu yense kunka ku hema wake. Ndipo Yowabu anabwerera kunka ku Yerusalemu kwa mfumu.
Pamenepo Yoramu anaoloka kunka ku Zairi, ndi magaleta ake onse pamodzi naye; nauka iye usiku, nakantha Aedomu akumzinga ndi nduna za magaleta, nathawira anthu kwa mahema ao.
ndipo anene kwa akulu a mzinda wake, Mwana wathu wamwamuna uyu ngwopulukira ndi wopikisana nafe, wosamvera mau athu, ndiye womwazamwaza, ndi woledzera.
Pamenepo amuna onse a mzinda wake amponye miyala kuti afe; chotero muchotse choipacho pakati panu; ndipo Israele wonse adzamva, nadzaopa.
Ndipo kunali, nthawi yakulowa dzuwa, Yoswa analamulira kuti awatsitse kumitengo; ndipo anawataya m'phanga m'mene adabisala; naika miyala yaikulu pakamwa pa phanga, mpaka lero lomwe lino.
Ndipo anamuunjikira mulu waukulu wamiyala, wokhalako kufikira lero lino; ndipo Yehova anatembenuka kusiya mkwiyo wake waukulu. Chifukwa chake anatcha dzina lake la malowo, Chigwa cha Akori, mpaka lero lino.
Ndipo mfumu ya ku Ai, anampachika pamtengo mpaka madzulo; koma polowa dzuwa Yoswa analamulira kuti atsitse mtembo wake pamtengo; ndipo anauponya polowera pa chipata cha mzinda; naunjikako mulu waukulu wamiyala, mpaka lero lino.
Ndipo Afilisti anaponyana nao, nakantha Aisraele; iwowa nathawira, munthu yense ku hema wake; ndipo kunali kuwapha kwakukulu; popeza anafako Aisraele zikwi makumi atatu a oyenda pansi.