Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 17:2 - Buku Lopatulika

ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo ndidzamgwera ali wolema ndi wofooka, ndi kumuopsa; ndi anthu onse amene ali naye adzathawa; pamenepo ndidzakantha mfumu yokha;

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono ndikamthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima, ndipo ndikamchititsa mantha. Anthu onse amene ali naye adzathaŵa. Pamenepo ine ndidzangopha mfumu yokhayo.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Ndipo ndikamuthira nkhondo atatopa ndiponso atataya mtima. Ndikamuchititsa mantha ndipo anthu onse amene ali naye akathawa. Ine ndikakantha mfumu yokhayo,

Onani mutuwo



2 Samueli 17:2
10 Mawu Ofanana  

Ndipo mfumu ndi anthu onse amene anali naye anafika olema; ndipo iye anadzitsitsimutsa kumeneko.


Ndipo Ahitofele ananena ndi Abisalomu, Ndiloleni ndisankhe tsopano anthu zikwi khumi ndi ziwiri, ndipo ndidzanyamuka usiku womwe uno ndi kulondola Davide;


Tsono mfumu ya Aramu idalamulira akapitao makumi atatu mphambu ziwiri za magaleta ake, niti, Musaponyana ndi anthu aang'ono kapena aakulu, koma ndi mfumu ya Israele yokha.


ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Koma olimawo m'mene anaona mwanayo, ananena wina ndi mnzake, Uyo ndiye wolowa; tiyeni, timuphe, ndipo ife tidzatenga cholowa chake.


Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.


kapena simuganiza kuti nkokoma kwa inu kuti munthu mmodzi afere anthu, ndi kuti mtundu wonse usaonongeke.


kuti anakomana ndi inu panjira, nakantha onse ofooka akutsala m'mbuyo mwanu, pakulema ndi kutopa inu; ndipo sanaope Mulungu.