Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:31 - Buku Lopatulika

31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

31 Pamenepo Yesu ananena kwa iwo, Inu nonse mudzakhumudwa chifukwa cha Ine usiku uno; pakuti kwalembedwa, Ndidzakantha mbusa, ndipo zidzabalalika nkhosa za gulu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

31 Pambuyo pake Yesu adaŵauza kuti, “Nonsenu mukhumudwa nane nkundisiya usiku uno. Paja Malembo akuti, ‘Ndidzapha mbusa, ndipo nkhosa za msambiwo zidzangoti balala.’

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

31 Pamenepo Yesu anawawuza kuti, “Usiku omwe uno inu nonse mudzandithawa, pakuti kwalembedwa: “ ‘Kantha mʼbusa, ndipo nkhosa zidzabalalika.’

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:31
16 Mawu Ofanana  

Ondikonda ndi anzanga apewa mliri wanga; ndipo anansi anga aima patali.


Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.


Munandichotsera kutali wondikonda ndi bwenzi langa, odziwana nane akhala kumdima.


Koma kunakomera Yehova kumtundudza; anammvetsa zowawa; moyo wake ukapereka nsembe yopalamula, Iye adzaona mbeu yake, adzatanimphitsa masiku ake; ndipo chomkondweretsa Yehova chidzakula m'manja mwake.


Ndinaitana akundikondawo koma anandinyenga; ansembe ndi akulu anga anamwalira m'mzindamu, alikufunafuna zakudya zotsitsimutsa miyoyo yao.


Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo.


Ndipo wodala iye amene sakhumudwa chifukwa cha Ine.


Mwana wa Munthu achokatu, monga kunalembedwa za Iye; koma tsoka ali nalo munthu amene Mwana wa Munthu aperekedwa ndi iye! Kukadakhala bwino kwa munthuyo ngati sakadabadwa.


Koma izi zonse zinachitidwa, kuti zolembedwa za aneneri zikwaniridwe. Pomwepo ophunzira onse anamsiya Iye, nathawa.


Onani ikudza nthawi, ndipo yafika, imene mudzabalalitsidwa, yense ku zake za yekha, ndipo mudzandisiya Ine pa ndekha. Ndipo sindikhala pa ndekha, chifukwa Atate ali pamodzi ndi Ine,


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa