Zekariya 13:7 - Buku Lopatulika7 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Galamuka, lupanga, pa mbusa wanga, ndi pa munthu mnzanga wa pamtima, ati Yehova wa makamu; kantha mbusa, ndi nkhosa zidzabalalika; koma ndidzabwezera dzanja langa pa zazing'onozo. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Chauta Wamphamvuzonse akunena kuti, “Lupanga iwe, dzambatuka, ukanthe mbusa wanga. Ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine. Ndikutero Chauta Wamphamvuzonse. Kantha mbusa kuti nkhosa zimwazikane. Pamenepo ndidzakantha ndi anthu wamba omwe.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 “Dzambatuka iwe lupanga, ukanthe mʼbusa wanga, ukanthe munthu amene ali pafupi ndi Ine!” akutero Yehova Wamphamvuzonse. Kantha mʼbusa ndipo nkhosa zidzabalalika, ndipo ndidzatambalitsa dzanja langa kuwononga zazingʼono. Onani mutuwo |