Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 15:23 - Buku Lopatulika

Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

Ndipo dziko lonse linalira ndi mau okweza; ndipo anthu onse anaoloka, ndi mfumu yomwe inaoloka mtsinje wa Kidroni, ndipo anthu onse anaolokera ku njira ya kuchipululu.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Tsono anthu onse adayamba kulira mofuula pamene mfumu ndi otsatira ake ankapita. Choncho mfumuyo idaoloka mtsinjewo, ndipo anthu onse adamtsatira kupita ku chipululu.

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Anthu onse a madera ozungulira analira mofuwula pamene anthu onsewo amadutsa. Mfumunso inawoloka chigwa cha Kidroni, ndipo anthu onse anayenda kulowera ku chipululu.

Onani mutuwo



2 Samueli 15:23
12 Mawu Ofanana  

Ndipo Davide ananena ndi Itai, Tiye nuoloke. Ndipo Itai Mgiti anaoloka, ndi anthu ake onse, ndi ana aang'ono onse amene anali naye.


Ona ndidzaima pa madooko a m'chipululu kufikira afika mau ako akunditsimikizira ine.


Ndipo mfumu inanena ndi Ziba, Ulikutani ndi zimenezi? Nati Ziba, Abuluwo ndiwo kuti akaberekepo a pa banja lanu; ndi mitanda ya mikate ndi zipatso za m'dzinja ndizo zakudya za anyamata; ndi vinyoyo akufooka m'chipululu akamweko.


Ndipo anamchotsera Maaka amake ulemu wa make wa mfumu, popeza iye anapanga fanizo lolaula; ndipo Asa analikha fano lake, nalitentha ku mtsinje wa Kidroni.


Popeza tsiku lomwelo lakutuluka iwe ndi kuoloka mtsinje Kidroni, tadziwa ndithu kuti udzafadi, mwazi wako udzakhala pamutu wa iwe wekha.


Ndipo ansembe analowa m'kati mwake mwa nyumba ya Yehova kuiyeretsa, natulutsira kubwalo la nyumba ya Yehova zoipsa zonse anazipeza mu Kachisi wa Yehova. Nazilandira Alevi, kuzitulutsira kunja kumtsinje wa Kidroni.


Ndipo chigwa chonse cha mitembo, ndi cha phulusa, ndi minda yonse kufikira kumtsinje wa Kidroni, kufikira kungodya kwa Chipata cha Akavalo kuloza kum'mawa, ponsepo padzapatulikira Yehova; sipadzazulidwa, sipadzagwetsedwa konse kunthawi zamuyaya.


Ndipo masiku aja anadza Yohane Mbatizi, nalalikira m'chipululu cha Yudeya,


Pakuti uyu ndiye ananenayo Yesaya mneneri, kuti, Mau a wofuula m'chipululu, konzani khwalala la Ambuye, lungamitsani njira zake.


Ndipo mwanayo anakula, nalimbika mu mzimu wake, ndipo iye anali m'mapululu, kufikira masiku akudzionetsa yekha kwa Israele.


M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake.


Kondwani nao iwo akukondwera; lirani nao akulira.