Yohane 18:1 - Buku Lopatulika1 M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20141 M'mene Yesu adanena izi, anatuluka ndi ophunzira ake, kunka tsidya lija la mtsinje wa Kidroni, kumene kunali munda, umene analowamo Iye ndi ophunzira ake. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa1 Yesu atanena zimenezi, adapita ndi ophunzira ake kutsidya kwa kamtsinje ka Kedroni. Kumeneko kunali munda, ndipo adaloŵa m'menemo. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero1 Yesu atamaliza kupemphera, Iye anachoka ndi ophunzira ake ndi kuwoloka chigwa cha Kidroni. Kumbali inayo kunali munda wa Olivi, ndipo Iye ndi ophunzira ake analowamo. Onani mutuwo |
Ndipo mfumu inalamulira Hilikiya mkulu wa ansembe, ndi ansembe a gawo lachiwiri, ndi olindira pakhomo, atulutse mu Kachisi wa Yehova zipangizo adazipangira Baala, ndi chifanizo adazipangira Baala, ndi chifanizo chija, ndi khamu lonse la kuthambo; nazitentha kunja kwa Yerusalemu ku thengo la ku Kidroni, natenga phulusa lake kunka nalo ku Betele.