Baibulo la pa intaneti

Zotsatsa


Baibulo lonse Chipangano Chakale Chipangano Chatsopano




2 Samueli 12:6 - Buku Lopatulika

ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.

Onani mutuwo

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

ndipo adzabwezera mwa mwanawankhosayo ena anai, chifukwa anachita ichi osakhala nacho chifundo.

Onani mutuwo

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ndipo pa mwanawankhosayo abwezere ena anai, chifukwa chochita zotere, ndiponso popeza kuti analibe chifundo.”

Onani mutuwo

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

Iye ayenera kulipira mwana wankhosa wamkaziyo kanayi, chifukwa anachita chinthu chimenechi ndipo analibe chifundo.”

Onani mutuwo



2 Samueli 12:6
7 Mawu Ofanana  

Abwezereni lero lomwe minda yao, minda yao yampesa, minda yao ya azitona, ndi nyumba zao, ndi limodzi la magawo zana limodzi la ndalama, ndi tirigu, vinyo, ndi mafuta, limene muwalipitsa.


mwini dzenje azilipa; azilipa ndalama kwa mwini nyamayo, koma yakufayo ndi yake.


Munthu akaba ng'ombe, kapena nkhosa, nakaipha kapena kuigulitsa, azilipa ng'ombe zisanu pa ng'ombeyo, ndi nkhosa zinai pa nkhosayo.


koma ikapezedwa idzabwezera kasanu ndi kawiri; idzapereka chuma chonse cha m'nyumba yake.


kapena chilichonse analumbirapo monama; achibwezere chonsechi, naonjezepo, limodzi la magawo asanu; apereke ichi kwa mwini wake tsiku lotsutsidwa iye.


Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai.


Pakuti chiweruziro chilibe chifundo kwa iye amene sanachite chifundo; chifundo chidzitamandira kutsutsana nacho chiweruziro.