Luka 19:8 - Buku Lopatulika8 Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Ndipo Zakeyo anaimirira nati kwa Ambuye, Taonani, Ambuye, gawo limodzi la zanga zonse zogawika pakati ndipatsa osauka; ndipo ngati ndalanda kanthu kwa munthu monyenga, ndimbwezera kanai. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Koma Zakeyo adaimirira nauza Ambuye kuti, “Ambuye, ndithudi ndidzapereka hafu la chuma changa kwa amphaŵi. Ndipo ngati ndidalandira kanthu kwa munthu aliyense monyenga, ndidzamubwezera kanai.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Koma Zakeyu anayimirira ndipo anati kwa Ambuye, “Taonani Ambuye! Theka la chuma changa ndipereka kwa osauka ndipo ngati ndinamubera wina aliyense pa chilichonse, ndidzamubwezera mochulukitsa kanayi.” Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.