Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
2 Samueli 11:6 - Buku Lopatulika Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Atamva zimenezi Davide adatumiza mau kwa Yowabu kuti, “Umtumize Uriya, Muhiti uja, abwere kuno.” Yowabu adatumizadi Uriya kwa Davide. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide. |
Ukachita zabwino, sudzalandiridwa kodi? Ukaleka kuchita zabwino, uchimo ubwatama pakhomo: kwa iwe kudzakhala kulakalaka kwake, ndipo iwe udzamlamulira iye.
Ndipo pakufika kwa iye Uriya uja, Davide anamfunsa kuti, Yowabu ali bwanji? Ndi anthu ali bwanji? Ndi nkhondo ili bwanji?
Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;
Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.
Pomwepo iye anati, Ndinachimwa, koma mundichitire ulemu tsopano pamaso pa akulu a anthu anga, ndi pamaso pa Israele, nimubwerere pamodzi ndi ine, kuti ndikalambire Yehova Mulungu wanu.