Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:74 - Buku Lopatulika

74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

74 Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

74 Apo Petro adayamba kulumbira nkumanena kuti, “Mulungu andilange, munthu mukunenayu ine sindimdziŵa konse.” Nthaŵi yomweyo tambala adalira.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

74 Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!” Nthawi yomweyo tambala analira.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:74
19 Mawu Ofanana  

Ndipo musamaopa amene akupha thupi, koma moyo sangathe kuupha; koma makamaka muope Iye, wokhoza kuononga moyo ndi thupi lomwe muGehena.


Yesu anati kwa iye, Indetu ndinena kwa iwe, kuti usiku uno, tambala asanalire, udzandikana Ine katatu.


Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.


Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Ndipo Yesu ananena naye, Ndithu ndinena ndi iwe, kuti lero, usiku uno, tambala asanalire kawiri, udzandikana Ine katatu.


Koma anakana, nanena, Sindidziwa kapena kumvetsa chimene uchinena iwe; ndipo anatuluka kunka kuchipata; ndipo tambala analira.


Koma Petro anati, Munthu iwe, sindidziwa chimene uchinena. Ndipo pomwepo, iye ali chilankhulire, tambala analira.


Pamenepo Petro anakananso; ndipo pomwepo analira tambala.


Pakuti ndikadafuna kuti ine ndekha nditembereredwe kundichotsa kwa Khristu chifukwa cha abale anga, ndiwo a mtundu wanga monga mwa thupi;


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


Onse amene ndiwakonda, ndiwadzudzula ndi kuwalanga; potero chita changu, nutembenuke mtima.


Ndipo iye anati kwa amai wake, Ndalama zija mazana khumi ndi limodzi anakuberani zimene munatembererapo, ndi kunenanso m'makutu mwanga, taonani ndalamazo ndili nazo, ndinazitenga ndine. Pamenepo amai wake anati, Yehova adalitse mwana wanga.


Koma ife sitingathe kuwapatsa ana athu aakazi akhale akazi ao; pakuti ana a Israele adalumbira ndi kuti, Atembereredwe wakupatsa Abenjamini mkazi.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa