Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 26:73 - Buku Lopatulika

73 Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

73 Ndipo popita nthawi yaing'ono, iwo akuimapo anadza, nati kwa Petro, Zoonadi, iwenso uli wa iwo; pakuti malankhulidwe ako akuzindikiritsa iwe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

73 Ndipo patangopita kanthaŵi, anthu amene anali pamenepo adadza nauza Petro kuti, “Ndithu nawenso ndiwe wa gulu lomweli, tadziŵira kalankhulidwe kakoka.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

73 Patapita kanthawi pangʼono, amene anayimirira pamenepo anapita kwa Petro nati, “Zoonadi, ndiwe mmodzi wa iwo, popeza mayankhulidwe ako akukuwulula.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 26:73
8 Mawu Ofanana  

ndi ana ao analankhula mwina Chiasidodi, osadziwitsa kulankhula Chiyuda, koma monga umo amalankhula mtundu wao uliwonse.


Ndipo anakananso ndi chilumbiro, kuti, Sindidziwa munthuyo.


Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira.


Koma anakananso. Ndipo patapita kamphindi, akuimirirapo ananenanso ndi Petro, Zedi uli wa awo; pakutinso uli Mgalileya.


Ndipo anadabwa onse, nazizwa, nanena, Taonani, awa onse alankhulawa sali Agalileya kodi?


pamenepo anati kwa iye, Unene tsono Shiboleti; ndipo akati, Siboleti, osakhoza kutchula bwino, amgwira namupha padooko pomwe pa Yordani; ndipo anagwa a Efuremu nthawi ija, zikwi makumi anai mphambu ziwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa