Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Samueli 11:6 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Ndipo Davide anatumiza mawu awa kwa Yowabu: “Nditumizire Uriya Mhiti.” Ndipo Yowabu anamutumiza kwa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Lopatulika

6 Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Davide natumiza kwa Yowabu, nati, Unditumizire Uriya Muhiti. Ndipo Yowabu anatumiza Uriya kwa Davide.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Atamva zimenezi Davide adatumiza mau kwa Yowabu kuti, “Umtumize Uriya, Muhiti uja, abwere kuno.” Yowabu adatumizadi Uriya kwa Davide.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 11:6
12 Mawu Ofanana  

Ukanachita zabwino sindikanakulandira kodi? Koma tsopano wachita zoyipa ndipo tchimo likukudikira pa khomo pako, likufuna kukugwira; koma iwe uyenera kugonjetsa tchimolo.”


Mkaziyo anakhala woyembekezera ndipo anatumiza mawu kwa Davide kunena kuti, “Ine ndine woyembekezera.”


Uriya atafika kwa Davide, Davide anamufunsa za momwe analili Yowabu, za asilikali ndi momwe nkhondo inkayendera.


ndi Uriya Mhiti. Onse pamodzi analipo 37.


Wobisa machimo ake sadzaona mwayi, koma aliyense amene awulula ndi kuleka machimowo, adzalandira chifundo.


Ambuye akuti, “Anthu awa amandipembedza Ine ndi pakamwa pawo, ndi kundilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Kundipembedza kwawo ndi kwa chiphamaso. Amandipembedza motsata malamulo a anthu amene anaphunzitsidwa.


Koma iye anakana pamaso pawo nati, “Sindikudziwa chimene ukunena.”


Iye anakananso molumbira kuti, “Sindimudziwa munthuyu!”


Pamenepo anayamba kudzitemberera ndipo analumbira kwa iwo nati, “Sindimudziwa munthu ameneyo!” Nthawi yomweyo tambala analira.


Sauli anati, “Ine ndachimwa. Komabe, chonde mundilemekeze pamaso pa akuluakulu, anthu anga, ndiponso pamaso pa Israeli. Mubwerere nane kuti ndikapembedze Yehova Mulungu wanu.”


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa