Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.
2 Samueli 11:4 - Buku Lopatulika Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Davide anatumiza mithenga, namtenga iye; iye nabwera kwa iye, ndipo anagona naye, pakuti adachoka mumsambo; ndipo anabwereranso kunyumba yake. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Apo Davide adatuma amithenga kuti akamtenge mkaziyo. Iwo adabwera naye kwa Davide, ndipo Davideyo adagona naye. Nthaŵi imeneyo nkuti mkaziyo atangomaliza kusamba. Pambuyo pake mkazi uja adabwerera kunyumba kwake. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Ndipo Davide anatumiza amithenga kwa iye kukamuyitana. Batiseba anabwera kwa Davide ndipo anagona naye. (Nʼkuti mkaziyu atayeretsedwa ku masiku ake osamba). Kenaka anabwerera ku nyumba yake. |
Pamene anamuona iye Sekemu, mwana wake wamwamuna wa Hamori Muhivi, kalonga wa dzikolo, anamtenga nagona ndi iye, namuipitsa.
Ndipo panali zitapita izi, kuti mkazi wa mbuyake anamyang'anira maso Yosefe: ndipo mkaziyo anati, Gona ndi ine.
Pakuti iwe unachichita m'tseri; koma Ine ndidzachita chinthu ichi pamaso pa Aisraele onse, dzuwa lili nde.
Chomwecho njira ya mkazi wachigololo; adya, napukuta pakamwa, nati, Sindinachite zoipa.
Mkazi yemwe, mwamuna atagona naye, onse awiri asambe ndi madzi, nadzakhala odetsedwa kufikira madzulo.