2 Samueli 10:14 - Buku Lopatulika Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mudzimo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Tsono Aamoni ataona kuti Asiriya athaŵa, nawonso adathaŵa pofika Abisai, nakaloŵa mu mzinda. Apo Yowabu adaleka kumenyana ndi Aamoni, nabwerera ku Yerusalemu. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Aamoni atazindikira kuti Aaramu akuthawa, iwo anathawanso pamaso pa Abisai ndi kulowa mu mzinda. Nkhondo itatha, Yowabu anabwerera ku Yerusalemu. |
Ndipo kunali pofikanso chaka, nyengo yakutuluka mafumu, Davide anatumiza Yowabu, pamodzi ndi anyamata ake, ndi Aisraele onse; ndipo iwo anasakaza ana a Amoni, naumangira misasa yankhondo Raba. Koma Davide anatsalira ku Yerusalemu.
Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso.
Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.
za Aaramu, za Amowabu, za ana a Amoni, za Afilisti, za Amaleke, ndi zofunkha za Hadadezere, mwana wa Rehobu mfumu ya ku Zoba.
Ndipo Abisai mwana wa Zeruya anakantha Aedomu mu Chigwa cha Mchere zikwi khumi mphambu zisanu ndi zitatu.