Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




2 Samueli 23:18 - Buku Lopatulika

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Ndipo Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, anali wamkulu wa atatuwa. Iye natukula mkondo wake pa anthu mazana atatu nawapha, natenga dzina iye mwa atatuwa.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Tsono Abisai, mbale wa Yowabu, mwana wa Zeruya, ndiye anali mtsogoleri wa anthu makumi atatu aja. Ndiye adapha anthu 300 ndi mkondo wake, nakhala wotchuka ngati anthu atatu ena aja.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Abisai mʼbale wa Yowabu mwana wa Zeruya ndiye anali mtsogoleri wa anthu atatuwa. Iye anapha ndi mkondo ankhondo 300, choncho iyeyo anali wotchuka pakati pa anthu atatu aja.

Onani mutuwo Koperani




2 Samueli 23:18
11 Mawu Ofanana  

Koma anthu otsalawo anawapereka kwa Abisai mbale wake, amene anawandandalitsa cha kwa Amoni.


Ndipo pamene ana a Amoni anaona kuti Aaramu anathawa, iwonso anathawa pamaso pa Abisai, nalowa m'mzindamo. Ndipo Yowabu anabwera kuchokera kwa ana a Amoni, nafika ku Yerusalemu.


Davide natumiza anthu atawagawa magulu atatu, gulu limodzi aliyang'anire Yowabu, lina aliyang'anire Abisai, mwana wa Zeruya, mbale wa Yowabu, ndi lina aliyang'anire Itai Mgiti. Ndipo mfumu inanena ndi anthu, Zoonadi ine ndemwe ndidzatuluka limodzi ndi inu.


Ndipo analipo ana atatu a Zeruya, ndiwo Yowabu, Abisai ndi Asahele. Ndipo Asahele anali waliwiro ngati mbawala.


Koma Amasa sanasamalire lupanga lili m'dzanja la Yowabu; chomwecho iye anamgwaza nalo m'mimba; nakhuthula matumbo ake pansi, osamgwazanso, nafa iye. Ndipo Yowabu ndi Abisai mbale wake analondola Sheba mwana wa Bikiri.


Kodi iye sindiye waulemu mwa atatuwa? Chifukwa chake anali kazembe wao; ngakhale iyenso sadafikane ndi atatu oyamba.


Motero Yowabu ndi Abisai mbale wake adapha Abinere, popeza iye adapha mbale wao Asahele ku Gibiyoni, kunkhondo.


ndi alongo ao ndiwo Zeruya ndi Abigaile. Ndi ana a Zeruya: Abisai ndi Yowabu, ndi Asahele; atatu.


Ndipo wina akamgonjetsa mmodziyo, awiri adzachilimika; ndipo chingwe cha nkhosi zitatu sichiduka msanga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa