2 Samueli 23:17 - Buku Lopatulika17 Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201417 Nati, Ndisachite ichi ndi pang'ono ponse, Yehova; ndimwe kodi mwazi wa anthu awa anapitawa ndi kutaya moyo wao? Chifukwa chake iye anakana kumwa. Izi anazichita ngwazi zitatuzi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa17 nati, “Ndithudi pali Chauta, sindingachite chinthu chotere, chifukwa kukhala ngati kumwa magazi a anthuŵa amene adaika moyo wao paminga.” Motero adakana kumwa madziwo. Zimenezi ndizo adachita anthu atatu amphamvu aja. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero17 Iye anati, “Inu Yehova, musalole kuti ine ndichite chinthu ichi! Kodi awa si magazi a anthu amene anayika miyoyo yawo pachiswe?” Ndipo Davide sanamwe madziwo. Zimenezi ndi zimene anachita anthu amphamvu atatuwo. Onani mutuwo |