2 Samueli 20:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze mizinda ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Davide anati kwa Abisai, Tsopano Sheba mwana wa Bikiri adzatichitira choipa choposa chija cha Abisalomu; utenge anyamata a mbuye wako numtsatire, kuti angapeze midzi ya malinga ndi kupulumuka osaonekanso. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Pamenepo Davide adauza Abisai kuti, “Sheba, mwana wa Bikiri, adzativuta kwambiri kupambana Abisalomu. Tenga ankhondo anga mulondole Shebayo kuti angadzipezere mizinda yamalinga namativutitsa.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Davide anati kwa Abisai, “Tsono Seba mwana wa Bikiri adzatipweteka kuposa momwe Abisalomu anatichitira. Tenga asilikali a mbuye wako ndipo umuthamangitse, mwina adzapeza mizinda yotetezedwa ndi kutithawa ife.” Onani mutuwo |
Chifukwa chake tsono nyamukani, mutuluke, nimulankhule zowakondweretsa anyamata anu; pakuti ndilumbira, Pali Yehova, kuti mukapanda kutuluka inu, palibe munthu mmodzi adzakhala nanu usiku uno; ndipo chimenechi chidzakuipirani koposa zoipa zonse zinakugwerani kuyambira ubwana wanu kufikira tsopanoli.