2 Akorinto 13:10 - Buku Lopatulika Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa. Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Chifukwa cha ichi ndilembera izi pokhala palibe ine, kuti pokhala ndili pomwepo ndingachite mowawitsa, monga mwa ulamuliro umene Ambuye anandipatsa ine wakumangirira, ndipo si wakugwetsa. Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Ndikulemba zimenezi ndisanafike kwanu, kuti ndikadzafika, pasadzakhale chifukwa choti ndidzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mwaukali. Ambuye adandipatsa ulamulirowo kuti ndilimbitse mpingo, osati kuti ndiupasule. Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Nʼchifukwa chake ndimalemba zinthu zoterezi pamene ndili kutali, kuti ndikabwera ndisadzagwiritse ntchito ulamuliro wanga mokalipa, uwu ndi ulamuliro umene Ambuye anandipatsa kuti ndikukuzeni inu osati kukuwonongani. |
m'dzina la Ambuye wathu Yesu, posonkhana pamodzi inu ndi mzimu wanga, ndi mphamvu ya Ambuye wathu Yesu,
koma ndipempha kuti pokhala ndili pomwepo, ndisalimbike mtima ndi kulimbika kumene ndiyesa kulimbika nako pa ena, amene atiyesera ife monga ngati tilikuyendayenda monga mwa thupi.
(pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga);
Pakuti ndingakhale ndikadzitamandira kanthu kochulukira za ulamuliro (umene anatipatsa Ambuye kukumangirira, ndipo si kukugwetsera kwanu), sindidzanyazitsidwa;
Ndinanena kale, ndipo ndinena ndisanafikeko, monga pamene ndinali pomwepo kachiwiri kaja, pokhala ine palibe, kwa iwo adachimwa kale ndi kwa onse otsala, kuti, ngati ndidzanso sindidzawaleka;
Ndipo ndinalemba ichi chomwe, kuti pakudza ndisakhale nacho chisoni kwa iwo amene ayenera kukondweretsa ine; ndi kukhulupirira mwa inu nonse, kuti chimwemwe changa ndi chanu cha inu nonse.
m'mayeredwe, m'chidziwitso, m'chilekerero, m'kukoma mtima, mwa Mzimu Woyera, m'chikondi chosanyenga;
Umboni uwu uli woona. Mwa ichi uwadzudzule mokalipa, kuti akakhale olama m'chikhulupiriro,