Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.
1 Samueli 9:21 - Buku Lopatulika Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine? Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014 Ndipo Saulo anayankha nati, Sindili Mbenjamini kodi wa fuko laling'ono mwa Israele? Ndiponso banja lathu nlochepa pakati pa mabanja onse a fuko la Benjamini? Potero mulankhula bwanji mau otere ndi ine? Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa Saulo adayankha kuti, “Komatu ine ndine Mbenjamini, fuko laling'ono pakati pa mafuko onse a Aisraele. Kodi banja langa sindiye laling'ono kwambiri pakati pa mabanja a fuko la Benjamini? Chifukwa chiyani mukundilankhula zotere?” Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero Sauli anayankha, “Inetu ndine Mbenjamini, fuko lalingʼono la mafuko onse a Israeli, ndipo banja langa ndi lalingʼono pakati pa mabanja a fuko la Benjamini. Nanga nʼchifukwa chiyani mukunena zimenezi kwa ine?” |
Apo pali Benjamini wamng'ono, wakuwachita ufumu, akulu a Yuda, ndi a upo wao, akulu a Zebuloni, akulu a Nafutali.
Pamene Efuremu analankhula panali kunjenjemera; anadzikweza mu Israele; koma pamene anapalamula mwa Baala, anafa.
Chifukwa munthu aliyense wakudzikuza adzachepetsedwa; ndipo wakudzichepetsa adzakulitsidwa.
Kwa ine wochepa ndi wochepetsa wa onse oyera mtima anandipatsa chisomo ichi ndilalikire kwa amitundu chuma chosalondoleka cha Khristu;
Koma oipa ena anati, Uyu adzatipulumutsa bwanji? Ndipo anampeputsa, osakampatsa mtulo. Koma iye anakhala chete.
Nati Samuele, M'mene munali wamng'ono m'maso a inu nokha, kodi simunaikidwe mutu wa mafuko a Israele? Ndipo Yehova anakudzozani mfumu ya Israele.
Ndipo Davide anati kwa Saulo, Ine ndiye yani, ndi moyo wanga uli wotani, kapena banja la atate wanga lili lotani mu Israele, kuti ine ndidzakhala mkamwini wa mfumu?
Ndipo anyamata a Saulo analankhula mau awa m'makutu a Davide. Nati Davide, Kodi muchiyesera chinthu chopepuka kukhala mkamwini wa mfumu, popeza ndili munthu wosauka, ndi wopeputsidwa.
Ndipo Samuele anatenga Saulo ndi mnyamata wake, napita nao ku chipinda cha alendo, nawakhalitsa pamalo a ulemu pakati pa oitanidwa onse; ndiwo anthu monga makumi atatu.