1 Samueli 9:20 - Buku Lopatulika20 Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako? Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201420 Za abulu ako atatayika adapita masiku atatu, usalingalirenso iwowa; pakuti anapezedwa. Ndipo chifuniro chonse cha Israele chili kwa yani? Si kwa iwe ndi banja lonse la atate wako? Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa20 Musadandaule za abulu anu amene akhala akusoŵa masiku atatu apitaŵa, poti adapezeka kale. Kodi ndani amene Aisraele akumfunitsitsa? Kodi sindiwe ndi banja lonse la bambo wako?” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero20 Musadere nkhawa za abulu anu amene akhala akusowa masiku atatu apitawa, poti apezeka kale. Kodi Aisraeli onse akufunitsitsa ndani? Kodi si ndiwe ndi nyumba yonse ya abambo ako?” Onani mutuwo |